Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 160
Paphata pa Chichewa
Mpofunika timumangire mpanda.
Kumasano: Kumanda.
Chitsanzo: Anamupeza akuthyola mango kumasano.
Kumaso: Maliseche.
Chitsanzo: Analira koopsa atamumenya kumaso.
Kumasuka:
(a) Kuchita zinthu mosamangika.
Chitsanzo: (1) Muzichita zinthu momasuka. (2) Khalani
omasuka kufunsa funso lililonse.
(b) Mawuwa amanenedwa ndi munthu amene akuuza
anzake kuti akhoza kunyamuka.
Chitsanzo: Tsopano mukhoza kumasuka.
(c) Kupita kuchimbudzi, kudzithandiza, kubiba.
Chitsanzo: Zitawavuta, analowa patchire kuti akamasuke.
(d) Kusiyana nawo mavuto.
Chitsanzo: Ndipite ku Jubeki kuti ndimasuke ku
mavutowa.
Kumasuka:
(a) Kuchita zinthu mopanda manyazi.
Chitsanzo: Akunjira, khalani omasuka.
(b) Kubiba, kudzithandiza.
Chitsanzo: Apita kokamasuka.
Kumasula munthu:
(a) Kutulutsa munthu amene anamangidwa kundende,
kuchotsa zingwe zomwe munamumangira munthu.
Chitsanzo: Munthu anamangidwa uja wamasulidwa.
(b) Kuuza munthu kuti adzipita.
Chitsanzo: Nonse amene mwamaliza takumasulani.
159