Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 16
Paphata pa Chichewa
Banyira (basela): Zinthu zongowonjezera, pulaizi.
Chitsanzo: Atigula zambiri, apatseniko banyira (basela).
Basopo! Mawu amene anthu ena amanena akamafuna
kuchenjeza munthu kuti asamale chifukwa akhoza
kumumenya kapena kumuchita zoopsa.
Chitsanzo: Basopo! Ukachitanso zimenezi ndikuswa.
Batiza: Kuyamba kuchita nawo zinazake zomwe poyamba
sunkachita kapena kuchititsa munthu wina kuyamba
kuchita zimene sankachita poyamba. Mawuwa
amatanthauzanso mwambo womwe achipembedzo
amachita pomiza munthu māmadzi kapena kumuwaza
madzi monga chizindikiro choti munthuyo walowa
tchalitchi chawo.
Chitsanzo: Amakonda mowa ndi awa, koma anawabatiza
anzawowo.
Beba:
(a) Kusangalatsa kapena kukoma.
Chitsanzo: (1) Maunguwa akubeba. (2) Masewerawa
akubeba.
(b) Kufika pachimake.
Chitsanzo: Chibwenzi chawo chafika pobeba.
(c) Kukolera.
Chitsanzo: Kupizani motowo kuti ubebe.
Bembelezi: Munthu wamawu aakulu (abesi), Chilombo
chomwe chimasokosera kwambiri (chilombochi
chimakhala chakuda ndipo chimakonda kuboola mitengo
kapena matabwa.)
Chitsanzo: Akamayankhula amangokhala ngati bembelezi.
15