Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 159

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Anapunthwa moti anangotsala pang’ono kuluma pansi. Kulumana: Kukangana, kuyambana. Chitsanzo: (1) Ndinawapeza akulumana. (2) Akakhala ma- lo amodzi sachedwa kuyamba kulumana. (3) Anyamata okondana aja alumana. Kuluwika: Kulankhula mawu omwe anthu ena sangawamve msanga. Chitsanzo: Pamenepatu ndiye mwandikuluwika, kuwoloka moto n’kutani? Kum’thyapa: Kum’menya. Chitsanzo: (1) Ukapitiriza kuvuta ndikuthyapa! (2) Mwa- nayu ndi wofunika kum’thyapa. Kumaiwerenga: Kumayamba waganiza kaye. Chitsanzo: Usanayambe chibwenzi umafunika kuma- yamba waiwerenga kaye. Kumalikukutu: Kumanda. Chitsanzo: Masiku ano mitengo yatsala kumalikukutu kokha. Kumanga m’masamba: Kubisira munthu zinazake, kupusitsa, kunamiza. Chitsanzo: Anzanuwotu akumangani m’masamba. Kumangika: Kusamasuka, kunjatika, kuchita zinthu mwamantha. Chitsanzo: Musamangike, mukhoza kudya zimene mukufuna. Kumangira mpanda: Kuletsa kuyendayenda. Chitsanzo: Akachoka pano akumakaonana ndi anyamata. 158