Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 157
Paphata pa Chichewa
Kulowa m’manda: Kuikidwa m’manda, kumwalira.
Chitsanzo: Akazi awo analowa m’manda chaka chatha.
Kulowa m’maso: Kusowa choti ungatenge.
Chitsanzo: Ndikulephera kusankha chabwino, zandilowa
m’maso.
Kulowa m’mimba: Kukuopseza.
Chitsanzo: Akuchita zimenezi kuti angondilowa m’mimba.
Kulowa m’nthumba: Kuwononga ndalama.
Chitsanzo: Nyumba ija ndi imene yawalowa m’nthumba.
Kulowa m’nyumba: Kugonana.
Chitsanzo: Banja lawo linatha chifukwa mwamuna
sankalowa m’nyumba.
Kulowa mphepo: Kuyamba kuvutavuta, kusokonekera.
Chitsanzo: (1) Banja lawo lalowa mphepo. (2) Mukayamba
mwano mulowetsa mphepo m’banja mwanu.
Kulowa mphepo: Kuyamba kuvutavuta.
Chitsanzo: Tekinoloje ikupangitsa kuti mabanja ambiri
alowe mphepo.
Kulowa mphuchi: Kulowa matenda.
Chitsanzo: Moyo wathu wangolowa mphuchi.
Kulowa pansi: Kusayenda bwino kwa bizinezi kapena
zinthu zina. Mawuwa angagwiritsidwenso ntchito ponena
za kuchepa kwa makhalidwe abwino.
Chitsanzo: (1) Makhalidwe abwino akulowa pansi. (2)
Bizinezi yake ikulowa pansi. (3) Bizinezi yawo itayamba
kulowa pansi, m’golosale yawo munangotsala zinthu zo-
sadyedwa zokhazokha monga malezala, mabatani ndi
masingano.
156