Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 155

Paphata pa Chichewa Kulondola: (a) Kunena zoona. Chitsanzo: Mwanayu ndi amene akulondola, akuluwa alephera. (b) Kutsata. Chitsanzo: Ndimulondole mwana uja kumsika. Kulondoloza: (a) Kutsata nkhani. Chitsanzo: Amenewa ndi amene akulondoloza nkhani ija. (b) Kusaphonya. Chitsanzo: Ndinadziwa kuti ndilondoloza. Kulonga manja m’matumba: Kupisira m’matuma. Chitsanzo: Ndinawaona atalonga manja m’matumba. Kulonga ufumu: Kuika munthu kukhala mfumu. Chitsanzo: Pulezidenti apita kumwambo wolonga ufumu. Kulongolozana: Kukangana. Chitsanzo: Akumalongolozana ndi mwamuna wawo. Kulongosoka: Kukhala munthu wabwino, wakhalidwe, wochita zinthu mwanzeru. Chitsanzo: Anabereka ana 10, koma m’modzi yekha ndi amene ali wolongosoka. Kulongosola: (a) Kufotokoza. Chitsanzo: Talongosolani bwinobwino, amati chiyani? (b) Kuika zinthu m’malo mwake, kukonza zinthu. Chitsanzo: Ndabwera kuti ndidzalongosole zinthu. Kuloshoka: Kugwa. Chitsanzo: Denga lawo laloshoka. 154