Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 152
Paphata pa Chichewa
Kulembeka pachipumi: Kuonekera kwa onse.
Chitsanzo: (1) Nkwiyo wawo unalembeka pachipumi. (2) Si
bwino kumalola kuti umphawi wako uchite kulembeka pa-
chipumi.
Kulenga: Kuchepa.
Chitsanzo: Mwana amene uja akulenga, sangalimbane ndi
ine.
Kulera:
(a) Kusamalira.
Chitsanzo: (1) Mkazi amene uja adzamulera. (2) Makolowa
amadziwa kulera ana.
(b) Kutsata njira zothandiza kuti musabereke mwana.
Chitsanzo: Anayamba kulera kuti asamangotumbiza ana.
(c) Kukhwefuka.
Chitsanzo: Chingwechi chalera, mpofunika tichikungenso.
Kulerera pachilolo: Kulera monyengerera, kusasatitsid-
wa.
Chitsanzo: Mwanayu ndi wopusa chifukwa anamulerera
pachilolo.
Kulerera pachinena: Kulera mwana momunyengerera,
kusalera bwino mwana.
Chitsanzo: Ana awo aja amawalerera pachinena.
Kulewa: Kuzemba, kuzinda.
Chitsanzo: Akanapanda kulewa chibakeracho
akanamugulura mano.
Kuleza mtima: Kudekha, kudikira, kuchedwa kupsa mti-
ma.
Chitsanzo: Kuyendetsa galimoto kumafuna munthu wole-
za mtima.
151