Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 151

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Mtengwayu wayamba kuulavulatu mwano, mpaka kufika ponena kuti anabwerera banja osati ukapo- lo? Kulavulira khala lamoto: Kulalatira wina utakwiya kwambiri. Chitsanzo: Tiyeni tichokepo. Mmene akuyang’aniramo akhoza kutilavulira khala la moto. Kulawa zamchere: Kuchita zinazake zomwe sungafunen- so kuzisiya. Chitsanzo: Ndinadziwa kuti akadzangolawa zamchere sadzafunanso kusiya. Kulawa: (a) Kungoyamba pang’ono. Chitsanzo: Filimuyo sitinaionere mpaka kuimaliza. Anan- gotilawitsako pang’ono. (b) Kumwa mowa. Chitsanzo: Amakonda kuyankhula chingelezi akalawa. Kulefuka: Kufooka. Chitsanzo: (1) Zimene andiuza zandilefula. (2) Ndangolefu- kiratu! Kulekana: Kusiyana. Chitsanzo: Mavutowa ndilekane nawo. Kulekerera mwana: Kulera mwana momunyengerera, kusalera bwino mwana. Chitsanzo: Makolo anu anakulekererani, n’chifukwa chake munakula mopusa chonchi. Kulema: Kutopa. Chitsanzo: Analema ndi mavuto. 150