Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 149

Paphata pa Chichewa Kukusowa: Kufunitsitsa utaonana ndi munthu winawake. Chitsanzo: Wachikondi wanga ndamusowa. Kukutembenukira: Kusintha poyerayera, kukuukira. Chitsanzo: Tinagwirizana bwinobwino koma titafika ananditembenukira. Kukutumula: Kumenya koopsa, kusansa. Chitsanzo: (1) Akukutumulanitu! (2) Takutumulani mpha- sayo! Kukuyabwa: Kusakusangalatsa, kukukwana. Chitsanzo: Chizolowezi chanuchi chimandiyabwa. Kukuzolowera: Kusiya kukulemekeza. Chitsanzo: (1) Musandizolowere choncho, lero ndiku- masulani! (2) Ana amenewa ayamba kundizolowera. Kukwangula m’kamwa: Kudyera nyama. Chitsanzo: (1) Lero m’kamwa mwathu mwakwangukako. (2) Lero tiphe nkhuku kuti tikwanguleko m’kamwa. Kukwapatira: Kuika chinthu munkhwapa, kupana chin- thu ndi nkhwapa kuti chisagwe. Chitsanzo: Akwapatira kachikwama. Kukwatira chiwiri: Kukhala ndi akazi awiri, mitala. Chitsanzo: Bambowa anakwatira chiwiri. Kukwatiwa mwamlato: Kukwatiwa kapena kuchita chinachake mtima uli kwina. Chitsanzo: Anangokwatira mwamlato, mkazi uja samufuna. Kukwawa kukaona abale: Kuyendera achibale, kupita malo ena. Chitsanzo: (1) Ndikufuna ndikwawire kumudziku kuti 148