Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 148
Paphata pa Chichewa
Kukumaliza: Kukusangalatsa.
Chitsanzo: Nyimboyi imandimaliza.
Kukumana nazo: Kukumana ndi mavuto.
Chitsanzo: Akapitiriza utambwali akumana nazo.
Kukunkha: Kutolera zinthu zotsalira.
Chitsanzo: Ndikupita kukakunkha m’munda wa agogo.
Kukunthumula: Kumenya.
Chitsanzo: Amukunthumula anzake.
Kukupanga kanyenya: Kukupweteka.
Chitsanzo: Usamale nawo anthu amene aja ndi zi-
gawenga. Akhoza kukupanga kanyenya.
Kukuphonya: Kusakumana nazo, kusemphana nazo.
Chitsanzo: Nkhani imeneyi inandiphonya.
Kukuponya miyala: Kukutaya, kusiya kukuthandiza.
Chitsanzo: Ayamba kutiponya miyala chifukwa choti ta-
sauka.
Kukupula:
(a) Kumenya.
Chitsanzo: Awakupula anzawo.
(b) Kuwaula khungu.
Chitsanzo: Anapsa ndi madzi otentha moti khungu lake
lakupuka.
Kukusa: Kuchititsa munthu kuti abwere kapena apita
malo enaake.
Chitsanzo: Ntchito ndi zimene zikukusa anthu kuti
abwere m’tauni muno.
Kukusira pamodzi: Sonkhanitsa, ika pamodzi.
Chitsanzo: Anthu onse ochedwa awakusira pamodzi.
147