Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 147

Paphata pa Chichewa chifukwa apolisi anali pomwepo. (2) Ndinawaona akumukukutira mano. Kukukwana: Kutopa nazo, kusasangalala ndi chinthu. Chitsanzo: (1) Nkhani imeneyi yandikwana. (2) Khalidwe lanuli landikwana. Kukula chiwindi: Kuchita makani. Chitsanzo: M’gowelo muno sitifuna mwana wokula chiwindi. Kukula mopulukira: Kukula mopusa, kusakula ndi kha- lidwe labwino. Chitsanzo: Makolo akamapanda kukwapula mwana, mwa- nayo amakula mopulukira ngati nkhuku yavetenale. Kukula movutikira: Kukula ndi moyo wovuta kwambiri. Chitsanzo: Ana amene anakula movutikira amakhala opanda chibwana. Kukula mtima: Kuchita makani. Chitsanzo: Kuno sitifuna mwana wokula mtima. Kukula mutu: Kusowa chochita. Chitsanzo: (1) Mutu wanga wakula, ndikusowa choti ndingachite. (2) Mavuto akakugwera umakula mutu. Kukulira m’chitukutuku: Kukula mopusa. Chitsanzo: Ana omwe anakulira m’chitukutuku, amalephera ndi kuphika komwe. Kukulowa: Kukuzolowera kwambiri, kusiya kukupats ale- mu. Chitsanzo: Anthu amenewa asandilowe chonchoyi! Kukulunga nsima: Kuphika nsima. Chitsanzo: Koma ndiye nsimayi mwaikulungatu. 146