Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 146
Paphata pa Chichewa
Kukonkha kukhosi: Kumwa.
Chitsanzo: Tipatseni thobwalo tikonkheko kukhosi.
Kukonza:
(a) Kupha
Chitsanzo: Tikufuna mukatikonzere nkhukuyi.
(b) Kumukhaulitsa, kumenya.
Chitsanzo: Zikuoneka kuti amukonza, watuluka m’nyum-
bamo misonzi ili chuchuchu.
Kukucheka ndi maso: Kuyang’ana mwamwano.
Chitsanzo: Amawayang’ana mowacheka ndi maso.
Kukucheza: Kukunyoza, kukuchititsa manyazi.
Chitsanzo: Anzanu aja ndiye akuchezanitu!
Kukuchita zina ndi zina: Kukumenya.
Chitsanzo: Sanatsike njinga pamene amadutsa pamanda.
Ndiye adzukulu atawaona, anawagwira n’kuwachita zina
ndi zina.
Kukujaira:
(a) Kuzolowera kwambiri.
Chitsanzo: Wajaira kukwera njinga.
(b) Kukuzolowera, kusiya kukulemekeza.
Chitsanzo: Anthu amenewa andijaira.
Kukukumba: Kukunena, kufukula mbiri yako yonse.
Chitsanzo: (1) Anabwera kudzandikumba. (2) Tiyeni tik-
umbe mbiri yawo. (3) Tsopano mwati mutikumbetu!
Kukukutira mano: Kukwiyira munthu koopsa.
Chitsanzo: (1) Atawaulula anyamatawo anayamba ku-
mukukutira mano, kungoti sanakamuchita zina ndi zina
145