Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 145

Paphata pa Chichewa phindu n’cholinga choti zinthu ziyambe kukuyendera bwino. Chitsanzo: (1) Ndipita kukagulitsa mandasiwa kuti ndikokere. (2) Lero ndipitanso kukagulitsa kuti ndikokere. Kukola chidwi: Kuchititsa chidwi kwambiri, kukopa. Chitsanzo: Nsalu yachikasuyo ndi imene yakola chidwi changa. Kukolera: (a) Kugwirira, kuyaka. Chitsanzo: Sipanatenge nthawi yaitali kuti motowo ukolere nkhalango yonse. (b) Kukwanira, kufalikira. Chitsanzo: (1) Tiyi wanuyu wakolera shuga. (2) Khalidwe limeneli lakolera mudzi wonse. Kukolezera moto (kusonkhezera): Kupangitsa kuti zi- nazake zichitike kwambiri kapena zifale. Chitsanzo: (1) Umphawi ndi umene ukukolezera moto kuti ana ambiri ayambe uhule. (2) Akuluakulu a boma ndi amene akusonkhezera anthu kuti azichita chiwawa. Kukoma mtima: Kukhala ndi mtima wabwino, kuchitira ena chifundo komanso kuwamvera chisoni. Chitsanzo: Mayiwa ndi wokoma mtima. Kukomedwa: Kusafuna kusiya chinthu, kutengeka ndi zinthu. Chitsanzo: Mayiwa ndi okomedwa. Kukondera: Tsankho. Chitsanzo: Mukugawa mokondera. 144