Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 144

Paphata pa Chichewa Kukodza pamphasa: Kukodza ukamagona. Chitsanzo: Anthu amene amakodzabe pamphasa atakula amakhala kuti ali ndi matenda. Kukoka chingwe: Kuimbira foni munthu wina. Chitsanzo: Mukamva kuti mayeso atuluka, mukhoza kungondikokera chingwe. Kukoka ng’ona: Kuyenda ndi munthu wachimasomaso, kutenga hule. Chitsanzo: Bambo uja anakoka ng’ona dzulo, komatu ali ndi mkazi kunyumba. Kukoka nkhani: Kusafuna kusiya nkhani, kapena kuiko- komeza. Chitsanzo: (1) Kuti anthu amene akwatirana akhale ndi banja losangalala amafunika kuyesetsa kuti asamakoke nkhani. (2) Achimwene anu aja ndi amene akuikoka nkhani. Kukoka phazi: Kuyenda mofulumira. Chitsanzo: Tiyeni tikoke phazi kuti tikafike kusanache. Kukokanakokana: Kukanganakangana. Chitsanzo: Anthu amenewa amakonda kukokanakokana. Kukokera pambali: Kupita penapake kuti mukakambirane. Chitsanzo: Ndinawakokera pambali kuti ndiwatsine khutu. Kukokera: (a) Kuchita zambiri. Chitsanzo: Tiyeni tilimbikire ntchito kuti tikokere. (b) Kupeza ndalama zambiri, kuchita zinthu kuti upeze 143