Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 143

Paphata pa Chichewa Kukhwefula: (a) Kufooketsa, kugwetsa mphwayi. Chitsanzo: Zimene andiuza zandikhwefula. (b) Kumasula pang’ono. Chitsanzo: Takhwefulani zingwezi. (c) Kuvalira buluku m’matako, kutsetseretsa buluku. Chitsanzo: Mnyamata wina wadutsa apa atakhwefula. Kukhwethemuka: Kufooka, kubwerera m’mbuyo. Chitsanzo: (1) Ng’ambayi yachititsa kuti alimi ambiri akhwethemuke. (2) Zimene mwanenazi zandikhwethemu- la. Kukhwima: (a) Kuzama pa nkhani ya zanyanga. Chitsanzo: (1) Mkulu ameneyu ndi wokhwima. (2) Anakwimira ana awo aja! (b) Kukula. Chitsanzo: Munthu amene akufuna kulowa m’banja ama- funika kudikira kuti akhwime bwinobwino. (c) Kucha. Chitsanzo: Chimanga chakhwima. (d) Kukhala oganiza bwino. Chitsanzo: Munthuyu ndi Nkhristu wokhwima. Kukhwimira panazale: Kulephera kupeza banja mpaka msinkhu wokhala pabanja utadutsa. Chitsanzo: Ukamangokana amuna ukhwimira panazale! Kukhwinyata: Kukhumata. Chitsanzo: Amafuna tizingokhala mokhwinyata. Kukodola: Kuitana. Chitsanzo: Akukukodola mnyamata uyo! 142