Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 142

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: (1) Mfumu itamwalira, anthu onse samagwira ntchito pokhudza maliro a mfumuyo. (2) Tikupita kukakhudza maliro. Kukhulula: (a) Kungochita zinthu mpaka pamapeto. Chitsanzo: Ndinamuuza kuti awerenge ndime imodzi, ko- ma iye wangokhulula mpaka kumapeto. (b) Kuchotsa ulusi umene unazengerezedwa, kusolola ulusi pa chinthu, kumasula chingwe. Chitsanzo: Wandikhululira juzi yanga. Kukhuta ngati chubu: Kukhuta kwambiri. Chitsanzo: Akakwiya amadya mpaka kukhuta ngati chubu. Kukhutchumula: (a) Kumenya. Chitsanzo: Ukachita masewera akukhutchumula. (b) Kutekesa chinthu mwamphamvu, kugwedezeka, ku- menyetseka. Chitsanzo: (1) Akukhutchumula thumba. (2) Akukhutchu- mula botolo la mowa. (3) Galimotoyo imangotikhutchumu- la. Kukhuthura nkhawa: Kuuza wina mavuto ako onse. Chitsanzo: Ndikufuna munthu woti ndimukhuthulire nkha- wa zanga. Kukhutira: Kukwanitsidwa ndi zimene uli nazo. Chitsanzo: Kumakhutira ndi zomwe uli nazo. Kukhuzumuka: Kudekha. Chitsanzo: (1) Mmene akukulamu mpamene akukhuzu- mukako, anali wovuta uyu! (2) Mwakhuzumukatu lero, chachitika n’chiyani? 141