Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 141
Paphata pa Chichewa
Kukhomera kudowa: Kusabereka.
Chitsanzo: Ambiri akaona kuti wina m’banja anakhomera
kudowa, amatuluka m’nyumba n’kupita kwina, kapena
kulowetsa fisi.
Kukhomereza: Kuthandiza wina kuti zimene ukumuuza
zimulowe mumtima, azimvetse.
Chitsanzo: Mawu awa muziwakhomereza mwa ana anu.
Kukhosi kuli bii:
(a) Usakusangalala.
Chitsanzo: Ndimadya nsimayo kukhosi kuli bii.
(b) Kuda nkhawa.
Chitsanzo: Nditangomva za nkhaniyo ndinangoti kukhosi
bii.
Kukhudula: Kumenya mwankhanza.
Chitsanzo: (1) Ukandiputanso ndikukhudula. (2)
Akungomwaza ndalama. Zikuoneka kuti wakatamuka.
Kukhudza mtima: Kukhudzika, kukhala ndi chisoni.
Chitsanzo: Nkhani imeneyi yandikhudza mtima.
Kukhudza:
(a) Kukhala ndi mlandu, kupezeka kuti unachita nawo
kapena ukufunika kuyankha pa nkhani inayake chifukwa
cha zimene unachita.
Chitsanzo: Atandiuza kuti nkhaniyo ikundikhudza
ndinawakanira kuti sikundikhudza.
(b) Kugwira chinthu.
Chitsanzo: Ndachulutsa masamba kuti ndisakhudze
nyansi.
(c) Kukhala pachisoni chifukwa cha maliro kapena vuto
lina lalikulu, kusiya zochita zina posonyeza chisoni.
140