Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 14

Paphata pa Chichewa Awapininga: Awalodza. Chitsanzo: Chilichonse sichikuyenda, zikungokhala ngati awapininga anzawo. Awatsekera: Amangidwa ndi apolisi. Chitsanzo: Anamenya akazi awo ndipo apolisi awatsekera. Azimu agwa m’mbale: Tachita mwayi. Chitsanzo: Apatu azimu ndiye atigwera m’mbale. Azungu: Amenewa ndi mawu achipongwe omwe anthu ena amatchura akamanena za ma alubino. Mawuwa ndi oletsedwa ndi mabungwe oona za ufulu wa anthu. Chitsanzo: Panali woimba wina wachizungu, ndipo kwawo kunali kwa Kabudula. 13