Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 139
Paphata pa Chichewa
Kukhala moyo wosalira zambiri: Kukhutira ndi zochepa
zimene uli nazo, kusakhala ndi chuma chambiri.
Chitsanzo: Anthu amene amakhala moyo wosalira zambiri
amasangalala.
Kukhala ndwii ngati akukumeta: Kukhala chete.
Chitsanzo: Musangotitu ndwii ngati akukumentani apa!
Kukhala phwi: Kungokhala pansi ngati chithumba.
Chitsanzo: Usangokhala phwi apa, tadzuka.
Kukhala thako limodzi: Kukhala mosakhazikika.
Chitsanzo: Pamudzi pano tangokhala thako limodzi.
Kukhala thako limodzi: Kusakhazikika.
Chitsanzo: Ife pamudzi pano tangokhala thako limodzi.
Kukhala: Kugwirizana ndi thupi lako, zinthu zomwe
zimaoneka bwino zikakhala limodzi, chinthu chomwe
ukachivala umaoneka nacho bwino. Tanthauzo lake le-
nileni ndi ndi kukhazika thupi pansi.
Chitsanzo: (1) Chovalachi chikukukhalani. (2) Akazi awo
aja amawakhala.
Kukhalira kulimba: Kukhala movutika kwambiri.
Chitsanzo: Moyowu ndi wovuta moti tikungokhalira kulim-
ba.
Kukhalira kupirira: Kukhala mozunzika.
Chitsanzo: Ukayamba kuona kuti pabanja ukukhalira
kupirira, umafunika kukumbukira kuti palibe anakutuma
kuti umulole.
Kukhalira manja: Kungokhala osachita chilichonse.
Chitsanzo: Ukakhalira manja udyanji?
138