Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 138
Paphata pa Chichewa
Kukankhira kunkhongo: Kusiya kuganizira nkhani ina-
yake, kunyalanyaza nkhani.
Chitsanzo: Musavutike nayo mtima nkhani imeneyi, in-
goikankhirani kunkhongo.
Kukantha: Kumenya.
Chitsanzo: Amukantha ndi chikuni.
Kukaswa miyala: Kukachita chimbudzi kapena kukabiba.
Chitsanzo: Angozungulira kuseriku, mwina apita kokaswa
miyala. Akanakhala akukataya madzi bwenzi atabwerako
kalekale.
Kukata: Kusiya, kutha. Amagwiritsidwanso ntchito aka-
manena zoti mvula yasiya kapena ikusiya.
Chitsanzo: Matenda pakhomo pano sakukata.
Kukatamuka: Kupeza ndalama zambiri.
Chitsanzo: (1) Mbala ngakhale aimenye, sivomera kuti
yaba ndalama chifukwa imadziwa kuti akangoimasula si
kukatamuka kwakeko! (2) Akungomwaza ndalama.
Zikuoneka kuti wakatamuka.
Kukazinga mowa: Kutcheza kapena kuphika mowa
wokoma.
Chitsanzo: Koma ndiye mwaukazingatu mowawu.
Kukhala limodzi: Kugonana.
Chitsanzo: (1) Zimakhala zochititsa manyazi kumakhala
limodzi ndi mtsikana musanakwatirane. (2) Zikuoneka
kuti anakhalapo limodzi.
Kukhala m’maluzi: Kukhala opanda ndalama.
Chitsanzo: Anthu ambiri ali m’maluzi.
137