Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 137

Paphata pa Chichewa Kukamulowerera mwamuna: Mawuwa amaneneda mtsi- kana akathawa kwawo n’kupita kumakakhala ndi mwamuna ukwati usanachitike. Chitsanzo: Mtsikana wofatsa uja anakamulowerera mwamuna. Kukana kali kutsaya: Kukana ukudziwa kuti wachita ndiwe, kukana pali umboni woti wachita ndiwe. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani ukukana kali kutsaya? Kukana kali kutsaya: Kukana ukudziwa kuti zimene akukufunsazo ndi zoona. Chitsanzo: (1) Bambowa akukana kali kutsaya. (2) Ata- mupezerera akuvuula ndiwo mumphika, anamufunsa kuti akutani, koma iye anayamba kukana kali kutsaya. Kukana kwam’tuwagalu: Kukanitsitsa. Chitsanzo: (1) Nditamupempha kuti andithandize kunyamula thumbalo, anandikanira kwam’tuwagalu. (2) Atamufunsa anakana kwam’tuwagalu. Kukang’antha: (a) Kumenya. Chitsanzo: Anamukang’antha ndi mtengo. (b) Kuvutika kwambiri, kusowa ndalama. Chitsanzo: Maluzi amukang’antha. Kukanjuta: Kukabiba, kukanyera. Chitsanzo: Alowa pachikangapo akukanjuta. Kukankha chikopa: Kudziwa kumenya mpira wa miyendo. Chitsanzo: Mwanayu amakankha chikopa. 136