Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 136

Paphata pa Chichewa amangokulondola. Kukakamira: Kusafuna kusiya kapena kuchoka. Chitsanzo: Mayiyu ndi wokakamira. Kukalamira: Kuyesetsa kuti upeze chinthu chinachake. Chitsanzo: Akukalamira kuti akhale mkulu wampingo. Kukamata: (a) Ena amatinso kupiringa mbamu. Chitsanzo: Uzikamata kaye mbamuyo usanasunse. (b) Kugwira. Chitsanzo: Apolisi amukamata, moti ali kundende. (c) Kuvutika kwambiri, kusowa ndalama. Chitsanzo: Maluzi amukamata koopsa. Kukamata: (a) Kugwira kapena kugwidwa. Chitsanzo: Apolisi amukamata akulowetsa katundu mwachinyengo. (b) Kungokhaliratu opanda ndalama. Chitanzo: Maluzi amukamata, n’chifukwa chake wapezeka pakhomo. (b) Kupiringa mbamu. Chitsanzo: Uzikamata bwinobwino mbamuyo. Kukamira: Kuwaza madzi ndi manja, kukuntha madzi m’manja. Chitsanzo: Mukutikamira inu! Osakutumulira uko bwanji manja anuwo! Kukamuka: Kuumako, kuchoka madzi. Chitsanzo: Yanikani zovalazi zikamukeko. 135