Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 135
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: Mashiniwa ajama.
(b) Kusokonekera mutu.
Chitsanzo: Mutu wanga wajama.
Kujegweda: Kudya.
Chitsanzo: Awa ntchito ndiye ayi, koma kujegweda.
Kujegweda: Mawu achipongwe onena za kutafuna.
Chitsanzo: Ndinawapeza akujegweda chimanga.
Kujejema: Kudodoma, kulephera kuchita zinthu bwinob-
wino.
Chitsanzo: (1) Amajejema poyankhula. (2) Akamanama
amajejema.
Kujiba: Kugwa chamutu kapena nsana, kugwa modetsa
nkhawa.
Chitsanzo: Mnyamata amakonda kuchita chiphindigoliro
uja wajiba ndipo wathyoka khosi.
Kujudula:
(a) Kukonza.
Chitsanzo: Ndikufuna akandijudulire foni yangayi.
(b) Kubera munthu.
Chitsanzo: Akuba amujudula katundu wake.
Kukaimirira: Kukabiba, kukachita chimbudzi kapena
kukakodza.
Chitsanzo: Adikireni pang’ono akubwera, apita kukaimiri-
ra.
Kukaimirira: Kupita kuchimbudzi, kukabiba, kukanyera.
Chitsanzo: Apita kukaimirira.
Kukakamira: Kusafuna kusiya chinthu chinachake.
Chitsanzo: Anyamata ambiri ndi okakamira, ukawakana
134