Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 134
Paphata pa Chichewa
Kuimika mphuno: Kufuna kumva fungo.
Chitsanzo: Ndayambira kalekale kuimika mphuno, koma
sindikumva zoti kuseriku kukuphikidwa kanthu.
Kuingitsa: Kuthamangitsa, kuchotsa.
Chitsanzo: (1) Ikapsa nsima amayamba kuingitsa anthu
kuti azipita kwawo. (2) Aziphunzitsi ndi amene akuingitsa
umbuli m’dziko muno.
Kuiphedule: Kuulula nkhani yachinsinsi.
Chitsanzo: Mwana wawo uja ndi amene waiphedula.
Kuiputa:
(a) Kuyamba kuchita chinachake monga kugwira ntchito.
Chitsanzo: (1) Mukuchedwa ndi chiyani, anzanutu aiputa
ntchito. (2) Kodi anzathu mwaiputa kale?
(b) Kulakwitsa chinachake.
Chitsanzo: Bambo atangondiyang’ana ndinadziwa kuti
ndaiputa.
Kuipweteka nsima: Kudya kwambiri nsima.
Chitsanzo: Koma ndiye taipwetekatu nsima.
Kuitolera: Kumvetsa zimene wina akunena, kulumikiza
zimene wina ananena kapena kuchita.
Chitsanzo: Ndaitolera tsopano, kodi ndi zimene amatan-
thauza?
Kujaira: Kuzolowera kwambiri.
Chitsanzo: (1) Wajaira kuyendetsa njinga. (2) Mukaman-
gomusekerera akujairani. (3) Galimoto simafuna anthu
ojaira.
Kujama:
(a) Kusiya kugwira ntchito.
133