Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 133

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: (1) Mwana wawo uja amamuhonga. (2) Anapita kukahonga kuti aziwanda. Kuijangirira: Kuchita zinthu mwadongosolo. Chitsanzo: Mukaijangirira nyumba imeneyi idzaoneka bwino. Kuika pamoto: Kuika pamavuto. Chitsanzo: Mukapanda kumuthandiza mwana wanuyu akuikani pamoto. Kuika: Kukwirira m’manda. Chitsanzo: Maliro aja anaika. Kuikirapo mtima: Kulimbikira. Chitsanzo: Anapambana chifukwa anaikapo mtima. Kuilumira mano: Kuichitira khama. Chitsanzo: Ntchito imeneyi kuilumira mano ingadzakupezetseni ndalama zambiri. Kuima mitu: Kusowa chochita. Chitsanzo: Nkhani imeneyi yandiimitsa mutu. Kuima: Kukhala ndi pakati. Chitsanzo: Mayi akaima, sayenera kumavala mabuluku. Kuimba lokoma: Kusangalala. Chitsanzo: Mphaka akachoka, khoswe amaimba lokoma. Kuimba sukulu: Kuphunzira sukulu. Chitsanzo: Ife sitinaimbe sukulu. Kuimika makutu: Kutchera khutu. Chitsanzo: Musanene chilichonse, anthu onse aimika ma- kutu! 132