Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 132
Paphata pa Chichewa
Kugwira nsewu: Kuyamba kuyenda bwino, kuzolowera
kuchita zinazake.
Chitsanzo: (1) Patenga nyengo kuti munthu ameneyu ag-
wire nsewu. (2) Ulimi wawo unagwira nsewu.
Kugwira nthawi: Kubwera kapena kuchita zinthu pa
nthawi yake.
Chitsanzo: (1) Aliyense adzagwire nthawi. (2) Amalawi
zimawavuta kugwira nthawi. (3) Ameneyu ndi munthu
wogwira nthawi.
Kugwira tambala kukamwa: Kulawirira.
Chitsanzo: Kuti tikafike nthawi yabwino, mpofunika
tigwire tambala kukamwa.
Kugwira: Kuyamba chibwenzi.
Chitsanzo: Wagwira kanjole kapamtundapo.
Kugwiririra: Kukakamiza munthu kuti ugone naye.
Chitsanzo: (1) Njonda ina imafuna kumugwiririra. (2)
Anasokonekera chifukwa anthu anamugwiririra ali mwa-
na.
Kugwiritsa kenakake: Kupatsa munthu ndalama kapena
zinthu zina.
Chitsanzo: (1) Bwerani mundithandize, ndikugwiritsani
kenakake. (2) Ayenera kukugwiritsa kenakake,
simungangogwira ulere!
Kuhonga: Kunyengerera munthu kuti achite zinazake.
Chitsanzo: Anthu ena amafuna kuwahonga kaye kuti
akuthandize kugwira ntchito.
Kuhonga: Kunyengerera munthu pomuchitira zabwino
kapena kumuchitira zinazake.
131