Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 131

Paphata pa Chichewa Kugwetsa nkhope: Kuchita manyazi. Chitsanzo: Pamene mwanayo amaulula zonse, bambowo anagwetsa nkhope. Kugwetsa: (a) Kutaya chinthu pansi mwadala kapena ayi. Chitsanzo: (1) Agwetsa foni. (2) Wagwetsa nyumba. (b) Kumaliza. Chitsanzo: (1) Tiyeni tigwetse ntchito. (2) Wagwetsa makapu awiri a mowa. Kugwidwa: Kukhala pachibwenzi, kufunsiridwa. Chitsanzo: Mtsikana ameneyutu anagwidwa kale, un- gawononge nthawi! Kugwintha: Mawu okokomeza komanso achipongwe onyoza munthu amene akudya. Chitsanzo: (1) Anawa safuna kugwira ntchito koma kugwintha. (2) Tazingogwinthani apa! Kugwira dzanja (nkono): Kuthandiza. Chitsanzo: Amenewa ndi amene anandigwira dzanja zinthu zitandivuta. Kugwira dzanja: Kuthandiza Chitsanzo: Sumachitira mwano munthu amene anakugwira dzanja. Kugwira mwendo: Kuchonderera, kupempha mochon- derera, kupepesa posonyeza kugonja. Chitsanzo: (1) Ndagwira mwendo wanu, ndithandizeni chonde! (2) Musandithamangitse bwana, ndagwira mwendo wanu! 130