Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 130
Paphata pa Chichewa
Kugwa mphwayi: Kufooka.
Chitsanzo: Musagwe mphwayi, mukhoza kupambana.
Kugwa nkhope: Kuchita manyazi chifukwa chodzudzu-
lidwa.
Chitsanzo: Ukamadzudzula mtsikana woyendayenda, sa-
magwa nkhope, koma amakutembenukira n’kuyamba ku-
kusambwadza.
Kugwa ulesi: Kufooka, kugwa mphwayi, kutaya mtima,
Kusiya kukopeka ndi chinthu.
Chitsanzo: (1) Nkhaniyi yandigwetsa ulesi. (2) Ndagwa
ulesi, basi sindipitakonso. (3) Nditazindikira kuti
ndalephera mayeso, ndinangogwa ulesi n’kuisiya sukulu.
Kugwa ulesi: Kufooka, kusiya kulimbikira.
Chitsanzo: Zimene anenazi ndi zimene zatigwetsa ulesi.
Kugwaza: Kupha mochita kubaya kapena kutema.
Chitsanzo: Akugwaza mkango m’thengomo.
Kugwedezeka (kutekeseka): Mawuwa amanenedwa zika-
khala kuti nkhani imene ili m’kamwam’kamwa ndi ya
munthu winawake, aliyense akungokamba za iye. Anga-
tanthauzenso kuti zinthu zinasinthiratu munthuyo atan-
gobwera.
Chitsanzo: Atangofika mudzi wonse unagwedezeka.
Kugwera: Kuchita zinazake mwamwayi.
Chitsanzo: Sikuti amandiposa bawo, lerolo wangogwera.
Kugwetsa misozi: Kulira.
Chitsanzo: Ndinalephera kudzigwira moti ndinagwetsa
misozi.
129