Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 13

Paphata pa Chichewa Atate: (a) Munthu wolemekezeka. Chitsanzo: Amenewa ndiye atate a pankhani zoimbaimba. (b) Bambo. Chitsanzo: Atate awo abwera mawa. Atengerepo phunziro: Aphunzirepo kanthu. Chitsanzo: Ndakhaulitsa enawa kuti enawo atengerepo phunziro. Athakati (nthakati): Afiti. Chitsanzo: M’mudzi muno mwachuluka athakati. Athupi: Wonenepa. Chitsanzo: Abale awo onse ndi athupi. Atisiya: Amwalira. Chitsanzo: Munthu amadwala uja watisiya. Atsibweni: Amalume, alongo awo a mayi. Chitsanzo: Kwabwera atsibweni anga. Auyamba ulendo: Anyamuka apita. Chitsanzo: Anzathu onse auyamba ulendo. Awachesula: Mawuwa amanenedwa ndi anthu omwe amakhulupirira za ufiti kuti wina walodza mnzake. Chitsanzo: N’chifukwa chiyani ukuchita makani? Akuchesula eti! Awadyetsa chibanzi: Awatseka pakamwa kuti asayankhule powapatsa chiphuphu. Chitsanzo: Zikuoneka kuti wolakwayo wawadyetsa chibanzi apolisiwo. 12