Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 128
Paphata pa Chichewa
Kugonera: Kudya. Tanthauzo lake lenileni ndi kugona
pamwamba pa chinachake.
Chitsanzo: Ife ndiye tangogonera mpunga.
Kuguguda mtima: Kukunyansa, kukuchititsa nseru.
Chitsanzo: Fungo limeneli likundiguguda mtima.
Kugulugusha: Kufuntha, kuvutitsa.
Chitsanzo: Mwanayu ndi wogulugusha.
Kugulukira: Kusokonekera. Mawu amene anabwera ku-
chokera ku zimene zimachitika mtedza ukakhalitsa
usanakololedwe. Umagulukira ndipo nthawi zambiri
umaonongekera pansi pomwepo. Umavutanso kukolola
chifukwa wambiri umatsalira pansi.
Chitsanzo: Ana awo onse ndi ogulukira.
Kugulula mano: Kumenya munthu kwambiri mwina
mpaka kumugulula mano.
Chitsanzo: Osamachita chibwana ndi amene uja akhoza
kukugulula mano.
Kugululira mano: Pusitsa.
Chitsanzo: Anthu oipa mtima anapita kwawo
n’kukamugulira mano.
Kugunda m’golo (kuomba m’golo): Kulephera.
Chitsanzo: Ana onse a pasukuluyi agunda m’golo.
Kugunda mwala: Kulephera.
Chitsanzo: Sindidzachitsanso masewera amenewa, nthawi
zonse ndimangogunda mwala.
Kugundika: Kutengeka ndi zinazake, kuchita zinazake
mwakhama kwambiri.
Chitsanzo: (1) Akagundika kuvina, simungamudziwe!
127