Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 127
Paphata pa Chichewa
Kugomera: Kusirira munthu kapena chinachake.
Chitsanzo: Ndimamugomera mnyamata amene uja.
Kugona (kugonana): Kuchita chiwerewere.
Chitsanzo: (1) Ngati ukufuna kuti matenda a bomawa
akuphonye, umafunika kupewa kumangogona ndi ali-
yense. (2) Munthu wanzeru samangogonana ndi aliyense.
Kugona mphika wapserera: Kugona pang’ono chifukwa
cha kanthu kena.
Chitsanzo: Timadikirira alendo moti lero tagona mphika
wapserera.
Kugona mutu uli kukhomo: Kugona mofunitsitsa kuti
kuche msanga.
Chitsanzo: Anthu onse omwe amapita kukagula chimanga
adagona mutu uli kukhomo.
Kugona ngati mvuu: Kugona mosalongosoka.
Chitsanzo: Achimwene anu amagona ngati mvuu. Akagona
ataloza uku, amadzuka ataloza kwinako.
Kugona tulo tofa nato: Kugona tulo tatikulu.
Chitsanzo: Ndi kale ndinagona tulo tofa nato.
Kugonekera khosi (kuthyolera khosi): Kusonyeza kuti
ukugwirizana nazo.
Chitsanzo: (1) Akayamba kunena zake zija osamugonekera
khosi. (2) Mtsikana akagonekera khosi amakhala kuti
wakulola.
Kugonekera khosi: Kuvomereza zimene wina akufuna.
Chitsanzo: (1) Ukamangogonekera khosi munthu aliyense,
ukumana ndi mavuto. (2) Amangogonekera khosi mnya-
mata aliyense.
126