Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 125
Paphata pa Chichewa
Kugamulira: Kupitira kutsogolo.
Chitsanzo: Ndimugamulira ameneyu!
Kugangalama: Kuvuta.
Chitsanzo: Bambowa ndi wogangalama.
Kuganiza mobwerera m’mbuyo: Kusaganiza bwino.
Kuti utukuke, umafunika nzeru osati kumaganiza mob-
werera m’mbuyo.
Kuganiza moperewera: Kusaganiza bwino.
Chitsanzo: Mayiwa amaganiza moperewera. Zoona osaona
kuti awatchera msampha.
Kuganiza mozondoka: Kusaganiza bwino.
Chitsanzo: Zimene amakamba ndi zambwerera. Zikuon-
eka kuti amaganiza mozondoka, apo ayi mawaya ena ana-
duka m’mutu mwake.
Kuganiza mwakuya: Kuganiza kwambiri.
Chitsanzo: (1) Usanasankhe zochita, uganize kaye
mwakuya. (2) Bambowa amaganiza mwakuya.
Kuganiza mwausiwa: Kusaganiza bwino.
Chitsanzo: (1) Anangoona kukula koma amaganiza
mwausiwa. (2) Munthu amadziwika ngati ali wanzeru
akatsegula pakamwa. Pamenepo mpamene umadziwa
munthu amene amaganiza mwausiwa.
Kugawana zida: Kulekana, kusiya kuchitira zinthu
limodzi.
Chitsanzo: (1) Kagulu koimba kaja kanagawana zida. (2)
Banja lija linagawana zida. (3) Mukapitiriza kukula mtima
tingogawana zida.
124