Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 124

Paphata pa Chichewa Kufuntha: Kuvutitsa. Chitsanzo: Mwanayu ndi wofuntha. Kufupa: Kupereka mphatso kwa munthu. Chitsanzo: Ndikufuna ndifupe akwati. Kufwafwantha: (a) Kumenya modetsa nkhawa. Chitsanzo: Atamugwira ali ndi mkazi wa mwini wake ana- mufwafwantha osati pang’ono. (b) Kunena bodza. Chitsanzo: Anzanu aja analifwafwantha bodza. Kufwichirira: Kusiya kukongola, kusintha maonekedwe. Chitsanzo: Koma ndiye mwafwichiriramotu m’taunimu, mumadya koma? Kugalika: Kumeza, kudya. Chitsanzo: Wagalika ndiwo yonse. Kugalukira: Kusiya kumvera, kupanduka. Chitanzo: Anthu ayamba kugalukira boma. Kugamphula: (a) Kuswa ndi manu. Chitsanzo: Tandigamphulireni mangolo. (b) Kugamphula chinthu. Chitsanzo: Ndani wagamphula khaka langa? Kugamuka: (a) Kugwa, kugumuka. Chitsanzo: Nyumba yawo yagamuka. (b) Ya ufaufa, yokoma. Chitsanzo: Aphika mbatata yogamuka. 123