Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 123
Paphata pa Chichewa
Kufera m’khwapa: Kukanikiratu kuchita chinthu monga
kuyankhula.
Chitsanzo: Pamlanduwo, wolakwayo sanayankhe
chilichonse moti anangofera m’khwapa.
Kufewa m’manja: Kupatsa.
Chitsanzo: Ukakhala wofewa manja, anthu amakuzolow-
era.
Kufika pamtima: Kukhudza mtima, kusangalatsa.
Chitsanzo: Mfundo zimene ananena zandifika pamtima.
Kufika pamtima: Kukhudzika, kukhala ndi chisoni.
Chitsanzo: Nkhani imeneyi yandifika pamtima.
Kufoila: Kupusa, kulephereka.
Chitsanzo: Asiyeni amenewa, ndi ofoila.
Kufuna kulowa pansi: Kuchita manyazi kwambiri.
Chitsanzo: Atandikalipira pamaso pa anzanga a kusuku-
lu, ndimafuna kulowa pansi.
Kufuna wopita naye (kufuna wotsagana naye): Ukufuna
wakufa naye.
Chitsanzo: (1) Samalani ndi mnyamata ameneyu, akungo-
funa wopita naye. (2) Samalani ndi mnyamata ameneyu,
akungofuna otsagana naye.
Kufunga: Kuyanga.
Chitsanzo: Maluwa aja anafunga pakhonde ponse.
Kufunsa chinyezi kubafa: Kufunsa zomwe ukudziwa
kale.
Chitsanzo: Zoona n’kumafunsa kuti wakuba amapita naye
kuti? Si kufunsa chinyezi kubafa kumeneko!
122