Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 122
Paphata pa Chichewa
Kudzukira kumanzere: Kusadzuka bwino.
Chitsanzo: Musamuyambe akhoza kukumenyani. Wadzu-
kira kumanzere lero.
Kufa choimirira: Kumagwirabe ntchito ukudwala. Ndiye
anthu akamachenjeza munthu wotero kuti akhoza kufa
akugwira ntchito amamuuza mawu amenewa.
Chitsanzo: Inutu mudzafa choimirira.
Kufa mphuno: Kusamva fungo.
Chitsanzo: Mwanayu ndi wakufa mphuno.
Kufa mutu:
(a) Kusokonekera chifukwa cha chikondi.
Chitsanzo: Kodi mwafa naye mutu mnyamata uja eti?
(b) Kusaganiza bwino.
Chitsanzo: Bambowa ndi akufa mutu.
Kufa ndi mseko: Kuseka kwambiri.
Chitsanzo: Ukamacheza ndi Mavuto, umafa ndi nseko
chifukwa pakamwa pake pamangobulika nthabwala zo-
khazokha.
Kufa ndi mtima: Kumalakalaka zinthu zomwe
sungazipeze.
Chitsanzo: Mukuganiza kuti mungagule galimoto,
mudzafa ndi mtimatu inu!
Kufa nsapato zili kuphazi: Kufa ukugwirabe ntchito
mwakhama.
Chitsanzo: Wandale uja anafa nsapato zili kuphazi.
Kufera fungo: Kulephera kupeza zimene ukufuna.
Chitsanzo: Nafenso zabwino timazifuna, koma tikungofera
fungo.
121