Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 121

Paphata pa Chichewa Kudzisinga: Kukhala chete osayankhula kanthu. Chitsanzo: Ukaona kuti ukhoza kupalamula umafunika kudzisinga. Kudzisunga: Kukhala osagonanan ndi munthu mpaka utalowa m’banja. Chitsanzo: Anthu amene amadzapeza banja labwino ama- khala amene ankadzisunga. Kudzitama: Kunyada, kutumbwa, kuyerekedwa. Chitsanzo: Munthuyu ndi wodzitama. Kudzitamandira: Kunena zimene amachita bwino komanso zomwe ali nazo, kudzitama. Chitsanzo: Amangokhalira kudzitamandira. Kudzithandiza: Kuchita chimbudzi, kubiba, kunyera. Chitsanzo: Koma anthu ndi aluso kwabasi, zoona kud- zithandiza pakati pansewu ngati pamenepa? Kudzithangata: Kukabiba, kukanyera. Chitsanzo: Walowa pachikanga kuti akadzithangate. Kudzivuta: Kudzivutitsa, kuchita zinthu zomwe sungapindulepo kanthu. Chitsanzo: Mwangodzivuta kubwera kuno. Kudziwonongera: Kudzibibira, kudzinyerera. Angatan- thauzenso kudzisanzira. Chitsanzo: Akumangodziwonongera, mwina akudwala m’mimba. Kudziyala: Kugona. Chitsanzo: Ndikatopa ndimangopita kukadziyala. 120