Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 120

Paphata pa Chichewa kudzimanga. (2) Ntchito ngati za apolisi, zimafuna anthu odzimanga. Kudzimangirira: Kudzipha podzimanga ndi chingwe, kudzikhweza. Chitsanzo: Mwana wawo anadzimangirira. Kudzimbuka: Kukwiya kwambiri mwadzidzidzi, kusintha poyerayera. Chitsanzo: Timacheza bwinobwino, koma titangotchula nkhani imeneyi anangodzimbuka. Kudzimva shuga (kudzimva uchi): Kuyerekedwa, kunya- da. Chitsanzo: Anthu akamamuyamikira amadzimva shuga. Kudzimva: Kuyerekedwa, kunyada. Chitsanzo: Bambo aja ndi wodzimva. Kudzinyenga: Kudzinamiza, kudzipusitsa. Chitsanzo: Ngati akuganiza kuti apambana akungodziny- enga. Kudzipachika (kupachikana): Kudziika pamavuto. Chitsanzo: Apa ndiye mwadzipachikatu, zoona kuulula nkhani yopusa ngati imeneyo! Kudzipepesa: Kudya moti umveko bwino. Chitsanzo: Ndagwira ntchito mwakhama, tsopano mpo- funika kuti ndidzipepese. Kudzipopa: Kuchita matama, kunena zambiri zokhudza iweyo, kudzichemerera. Chitsanzo: Mnyamata wake ndi wodzipopa, amangokha- lira kunena zimene amachita. 119