Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 12

Paphata pa Chichewa Anditembenukira: Andiukira. Chitsanzo: Mabwenzi anga onse anditembenukira. Anthanga imodzi: Omwe unabadwa nawo limodzi. Chitsanzo: Anzanga onse anthanga imodzi anakwatiwa. Anthu adera: Anthu osawadziwa, anthu omwe si abale ako. Chitsanzo: Sindingamathandize anthu adera abale anga akuvutika. Anyanya: Awonjeza. Chitsanzo: Amunanga anyanya nsanje. Aona mbwadza: Aona zoopsa. Chitsanzo: Akachita masewera aona mbwadza. Apo bii: Mawuna amanenedwa pofuna kutanthauza kuti, ngati zimenezi sizichitika ndichita zakutizakuti. Chitsanzo: Mubweretse ndalama zanga, apo bii sindikupatsani katundu wanuyu. Apo phuluzi: Zikangolephereka zimenezi uona zakutizakuti. Chitsanzo: Ubweretse ndalama zanga, apo phuluzi, ndikupha. Asukusula: (a) Achenjera. Chitsanzo: Tsopano asukusula moti ayamba kutinyoza. (b) Kutsuka m’maso, kutsuka nkhope ukangodzuka kumene. Chitsanzo: Ndipatseni madzi ndisukusule. 11