Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 119

Paphata pa Chichewa Kudzikhweza: Kudzipha podzimangirira. Chitsanzo: (1) Alimi ambiri ataona kuti chimanga chawo chapserera ndi ng’amba, anangodzikhweza n’kufa. (2) Katundu wawo atapsa ndi moto wolusa, anangodzikhwe- za. Kudzikoka: Kuyenda movutikira. Chitsanzo: Amayenda modzikoka popita kuchipatalako. Kudzikumbira manda: Kuchita zinthu zomwe zikhoza kukubweretsera mavuto. Chitsanzo: Makutu a munthu akangotsekeka, amakhala kuti wayamba kale kudzikumbira manda. Kudzikuza: Kuyerekedwa, kunyada. Chitsanzo: Bambo aja ndi wodzikuza. Kudziletsa: Kupewa kuchita zinazake zimene umafuna. Chitsanzo: Munthu wokwatira amafunika kukhala wodziletsa pochita zinthu zina. Kudzilimbitsa: Kupirira, kuchita khama kuti usachite zi- nazake. Chitsanzo: Ingodzilimbitsani kuti musagone. Kudziluma: Kulephera kulankhula bwinobwino. Chitsanzo: Pamene amayankhula amangodziluma. Kudzimana: Kukhala moyo wovutikirapo mochita kusankha kuti uchite zinazake zofunika kwambiri. Ku- khala moyo wovutikirapo zili zoti ukanatha kukhala moyo wabwino kwambiri. Chitsanzo: Mkaziyu ndi wodzimana. Kudzimanga: Kudziletsa kuti usachite chinachake. Chitsanzo: (1) Thupi lako likayamba kuvuta, umafunika 118