Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 118

Paphata pa Chichewa n’kudzitosa nacho pathupi. Chitsanzo: Kuphunzitsa ana a sukulu zinthu zomwe sukuzidziwa kumakhala kudzibaya. Kudzichekenira: Kudzitama, kunena zabwino zimene umachita. Chitsanzo: Atsikana safuna mnyamata wodzichekenira. Kudzifufuza: Kuona bwinobwino zimene umalakwitsa, kuganizira zimene umachita. Chitsanzo: Udzifufuze bwinobwino kuti uone ngati uli ndi khalidwe loipa. Kudzigangira: Kusafuna kuuzidwa zochita, kudzitama. Chitsanzo: Mfumu imeneyi ndi yodzigangira. Kudzigobera manda: Kuchita zinthu zomwe zikhoza ku- kubweretsera mavuto. Chitsanzo: (1) Makutu a munthu akangotsekeka, ama- khala kuti wayamba kale kudzigobera manda. (2) Anayamba kale kufukula mwalawu ndipo lero wawaphin- ja. Sankadziwa kuti akudzigobera manda. Kudzigwira: Kudzilimbitsa mtima kapena kudziletsa kuti usachita zinazake. Chitsanzo: (1) Ndimafunika kudzigwira kuti ndisalire. (2) Anandipsetsa mtima, kungoti ndinangodzigwira kuti ndi- sawayankhe mwano. Kudziipitsira: Kuchitira chimbudzi m’kabudula, kud- zibibira, kudzinyerera. Chitsanzo: (a) Atakumana ndi fisiyo anangotsala pang’ono kudziipitsira. (b) Anamumenya kwambiri mpaka anad- ziipitsira. 117