Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 117

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: (1) Mtsikana ameneyu wadyetsa amuna ambiri uyu. (2) Amadyetsa kwa chikhwaya chapamtundapo. Kudyetsedwa khuzumule: Kusiya kuyendayenda, kufatsa. Chitsanzo: (1) Masiku ano amangoti zungulizunguli pa- nyumba yawo ngati anawadyetsa khuzumule. (2) Kufatsa kumeneku sanawadyetse khuzumule awa! Kudzadzada: (a) Kukhapa chinthu. Chitsanzo: (1) Zikungokhala ngati wina akundidzadzada ndi musi. (2) Amudzadzada ndi chikwanje. (b) Kumva kupweteka kwambiri. Chitsanzo: Thupili likundidzadzada. Kudzala: (a) Kukwirira munthu kumanda kapena kuika maliro. Chitsanzo: Bambo athu atamwalira tinabwera kuno ndipo tinawadzala m’manda awo. (b) Kudzadzitsa. Chitsanzo: Madzi adzala mgolo. (c) Kukwirira mbewu pansi kuti imere. Chitsanzo: Tikupita kukadzala chimanga. (c) Malo otayako zinyalala. Chitsanzo: Mukataye kudzala. Kudzandira: Kugwedezeka mofuna kugwa. Chitsanzo: Amadzandira pobwera konseku, koma atafika pamlathopa anadutsapo bwinobwino. Kudzibaya: Kuchita zinthu zodzipweteka wekha. Tan- thauzo lake lenileni ndi kutenga chinthu chakuthwa 116