Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 116
Paphata pa Chichewa
Kudyera masuku pamutu: Kuchenjeretsa.
Chitsanzo: (a) Anthu olemera amakonda kudyera anzawo
masuku pamutu. (b) Onse amagwira ntchito yofanana,
koma wina uja amamudyera mnzake uja masuku pamutu.
Kudyera nsima: Mawuwa amanenedwa potanthauza kuti
m’bale wako anamwalira. Tanthauzo lake lenileni ndi
kudya chinachake, makamaka ndiwo, limodzi ndi nsima.
Chitsanzo: Bola inu muli ndi agogo, athu tinadyera nsima.
Kudyera umo: Kukana cholakwa kotheratu.
Chitsanzo: Atamufunsa ngati waswa mphikawo, ananena
kuti wadyera umo.
Kudyerera maso: Kuyang’ana mosirira munthu.
Chitsanzo: Wayamba kudyerera maso mtsikana
wapamtunda uja.
Kudyerera: Kukhala ndi moyo nthawi yaitali, kusangala-
la.
Chitsanzo: (1) Mwanayu wafa asanadyerere. (2) Mpo-
funika tidyerere ndalama tapangazi. (3) Muziyendetsa
bwino galimoto, sindinadyerere.
Kudyetsa: Tanthauzo lake lenileni ndi kutenga chakudya
n’kumaika m’kamwa mwa munthu wina.
(a) Kukambira munthu wina nkhani.
Chitsanzo: Ndinawapeza atatangandidwa ndikudyetsa
tinkhani tawo tabodza.
(b) Kuchititsa kuti ena atenge chinthu kapena ndalama
zako. Zimakonda kuchitika pochita masewera.
Chitsanzo: Wadyetsa ndalama zake zonse ku juga.
(c) Mkazi kumagona ndi mwamuna kapena amuna.
115