Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 115
Paphata pa Chichewa
Kudya ziro: Kulephera zonse. Mawu amenewa amakonda
kugwiritsidwa ntchito kusukulu.
Chitsanzo: Anzake onse a m’kalasi adya ziro.
Kudya:
(a) Kulowetsa chakudya m’mimba.
Chitsanzo: Ndikudya chimanga.
(b) Kukhoza.
Chitsanzo: Mwana wanu wadya ziro.
Kudyaka: Kuponda.
Chitsanzo: Mwana wadyaka nsomali.
Kudyakwathu: Zimene timachita, zimene tinazolowera.
Chitsanzo: Masewera ampira ndiye kudyakwathu.
Kudyana:
(a) Anthu oyandikana nyumba onse akakweza kwambiri
zoimbira zawo pamalopo n’kumamveka chiphokoso
chosamveka bwinobwino.
Chitsanzo: Magetsi akangoyaka, anthu a m’nyumba zonse
zili apazi amayatsa zoimbira zawo ndipo nyimbo
zimadyana.
(b) Kuyambana, kukangana.
Chitsanzo: Mmene ndimadutsa pamalopo panali pali
pokopoko, kaya sadyana kaya.
(c) Kugundana.
Chitsanzo: Galimoto yawo inadyana ndi galimoto ya apoli-
si, moti awatsekera.
Kudyeka ndi mafupa omwe: Kugonja kotheratu.
Chitsanzo: (1) Sadyeka anadyeka ndi mafuma omwe. (2)
Amayerekedwa, lero wadyeka ndi mafupa omwe.
114