Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 114

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: Ataona kuti mavuto amupanikiza, anangogani- za zodya mpamba. Kudya mtedza waching’onga: Kuiwalaiwala. Chitsanzo: Mungawauze zinthu n’kumaganiza kuti azisunga? Anadyatu mtedza waching’onga. Kudya mtima wa sontho: Kufulumira kuyankhula kapena kuchita kanthu, kusaugwira mtima, kupupuluma. Chitsanzo: Mwana wanuyu anadya mtima wa sontho. Sa- funa nkhani imudutse. Kudya mutu: Kuganiza kwambiri, kapena kuganizira nkhani inayake. Chitsanzo: (a) Ngati ukufuna kupeza yankho lolondola, uyenera kudya mutu. (b) Usanavomere, umafunika kuyamba wadya kaye mutu. Kudya nauzira: Kuyesa kukometsa zinazake n’cholinga choti upindulepo. Chitsanzo: Pofuna kuti asasankhe chitenje chabwinocho, anamulozera china. Amene uja ndi wachinyengo kwambi- ri, amadya nauzira. Kudya nthawi: Kugwiritsa ntchito nthawi yopitirira pa imene unauzidwa, kuwononga nthawi. Chitsanzo: (1) Zimene mukuchitazi zikungodya nthawi. (2) Mkuluyutu wadya nthawi. Kudya wani: Kuchita zakupsa, kukhala patsogolo. Chitsanzo: Anyamata akuno ndi amene anadya wani pampikisanowo. Kudya zankhuli: Kudyera nyama. Chitsanzo: Ndikufuna kudya zankhuli. 113