Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 113

Paphata pa Chichewa Kudya kam’lupsa: Kulawa zoipa, kuzolowera zoipa. Chitsanzo: Mwana ameneyu anaipira kudya kam’lupsa. Kudya kuwo: Kuchenjeretsa. Mawuwa anabwera poten- gera zimene zimachitika anthu akamayenda bawo, mun- thu akamudya mnzake mulu waukulu wa nkhomo. Chitsanzo: Pamenepa ndiye akudyani kuwotu, kukuten- gerani mpani ndi mbewa zomwe! Kudya m’mphunom’mphuno: Kudya mofulumira kwam- biri komanso kudya zakudya zambiri nthawi imodzi, ena amati kudya monthunthumira. Chitsanzo: (a) Osamadya m’mphunom’mphuno ngati ukuthawa. (b) Anthu omwe amadya m’mphunophuno amachititsa manyazi. Kudya milomo: Chichewa chamakono chonena za kupsopsona munthu kapena kumukisa. Chitsanzo: (1) Anawapeza akudyana milomo. (2) Ndikufu- na kudya milomo. Kudya miseche: Kunena zoipa za munthu wina. Chitsanzo: Ndikudziwa kuti ndikangochoka muyamba kundidya miseche. Kudya moto: (1) Kukwiya. Chitsanzo: Atayankhula mawu amwano, mwamuna wake anadya moto. (2) Kuchita bwino kwambiri. Chitsanzo: Gulu la mudzi wathu ndi limene linadya moto pampikisanowo. Kudya mpamba: Kuwononga ndalama za bizinezi. 112