Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 111
Paphata pa Chichewa
Chitsanzo: (1) Ndikamayankhula amangondidula pa-
kamwa. (2) Musawadule pakamwa, asiyeni amalizitse.
Kudula phazi: Kusiya kupita pakhomo kapena malo
enaake.
Chitsanzo: (1) Chiamanire mchere, anangodula phazi
pakhomo pano. (2) Nditaona kuti sakundiyang’ananso ndi
diso labwino ndikapita kwawo, ndinangodula phazi.
Kudula waya: Kuthawa.
Chitsanzo: Chigawenga anachigwira chija chadula waya.
Kudula: Kuthamanga kwambiri. Mawuwa amatanthau-
zanso kugwetsa chinachake pochikhapa kapena ku-
chicheka.
Chitsanzo: Mwana uyu amadula osati masewera, akhoza
kuthamanga kupita kunsika n’kubwerako isanathe 30
minitsi.
Kudulira mkuzi: Kuthamangitsa munthu pakhomo, kusi-
ya kuthandiza wachibale kapena mwana.
Chitsanzo: Choka pakhomo pano, takudulira mkuzi.
Kudulizira: Kupitira kutsogolo, kutseka njira.
Chitsanzo: (1) Sindivutika ndi kudzera uku,
ndingodulizira. (2) Kuti ndimugwire, ndingomudulizira.
Kudushula:
(a) Kumenya.
Chitsanzo: Anzake amudushula.
(b) Kuchotsa munthu penapake.
Chitsanzo: Mabwana akudushula anthu onse omwe
amachita unyizi akamagwira ntchito.
110