Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 110

Paphata pa Chichewa Kudikula: Kuvina. Chitsanzo: Msonkhanowo utafika pachiindeinde, pulezidenti anayamba kudikula. Kudilizika: (a) Kutha kapena kusokonekera kwa bizinezi. Chitsanzo: (a) Ankakhala ndi ndalama bizinezi yake isanadilizike. (b) Katundu wawo atangopsa ndi moto, bizinezi yawo inadirizika. (b) Kugwa kwa nyumba chifukwa cha chinyezi kapena ku- salimba kwa maziko. Chitsanzo: Nyumba yake yadilizika. Kudokonya: Kutosa ndi mtengo kapena chinthu china. Chitsanzo: (1) Ndinamuona akudokonya mapapaya osapsa. (2) Mutenge ndondo ndipo muzidokonya aliyense amene akuwodzera. Kudolola: Kukopa. Chitsanzo: Wakudololanitu mkaziyu. Kududuluza: Kukankha, kapena kukoka mochita kuka- kamiza. Chitsanzo: Anachita kumunduduluzira paja. Kuduka: Kutha kapena kusokonekera kwa bizinezi. Chitsanzo: (1) Mukufuna bizinezi yanga iduke? (2) Poyamba ankagulitsa mandasi koma anaduka. Kudula ngati zitsulo zandege: Mawuwa amanenedwa chinthu chimene ukugula chikakhala chodula kwambiri. Chitsanzo: Matimati akudula ngati zitsulo zandege. Kudula pakamwa: Kuyamba kuyankhula wina ali mkati moyankhula, kusiyitsa wina kuyankhula. 109