Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 11

Paphata pa Chichewa Anakhala bwanji: Kodi munthu ameneyu ndi wotani? Chitsanzo: (1) Anakhala bwanji munthu? Ndi wovuta kumumvetsa, akachita choipa savomera. (2) Kodi mayi amenewa anakhala bwanji? Zoona osachita manyazi ndi anthu onsewa! Anakhulana: Anayambana. Chitsanzo: Anthuwa akuoneka kuti anakhulana. Anamuchotsa mbola: Anamuthetsa makani, anafatsa. Mawuwa anachokera ku zimene njuchi imachita. Kungoichotsa mbola kapena ikangoluma kamodzi, imakhala yoti singachitenso kanthu. Chitsanzo: Masiku ano anafatsako, anzake anamuchotsa mbola. Anamulowa mumtima: Anamufika pamtima, anamva chisoni. Chitsanzo: Mawu anamuuzawo anamulowa mumtima. Anamwa tiyi adzamwanso: Zinthu zimasintha, mavuto amatha. Chitsanzo: Mukavutika musamataye makapu, anamwa tiyi adzamwanso. Anandikhula: Anandimana. Chitsanzo: Nditawapempha adangondikhula. Ananditsukuluza: Anandilalatira. Chitsanzo: Ukanamva chisoni ukanaona mmene ananditsukuluzira. Anangoti du: Samayankhula. Chitsanzo: Mmene timacheza, mnyamatayo anangoti du! 10