Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 109

Paphata pa Chichewa Kuda: (1) Kuipa, kunyansa. Chitsanzo: Sindingakwatire mkazi wakuda ngati amene uja. (2) Zamuvuta. Chitsanzo: Mmene zateremu ndiye kuti zamudera. Kudakhwira: Kupuma. Chitsanzo: Ngakhale tikumane ndi mavuto sitidandaula, bola tikudakhwira. Kudakwa: Kuledzera. Munthu amene amakonda kuledze- ra timamuti chidakwa. Chitsanzo: Anapapira mowawo ndipo posakhalitsa anago- na pansewu atadakwa. Kudampira: Kusambira, kudumphadumpha m’madzi. Chitsanzo: Tiyeni tikadampire. Kudekha: Kuugwira mtima, kusapupuluma. Chitsanzo: Anzanuwa ndi wodekha. Kudeweza: Kuderera. Chitsanzo: Umadeweza mphwanga, lero ndikuminitsa. Kudibwa: Kudyedwa. Chitsanzo: Chikhawo chimenechi chimadibwa. Kudidimuka: Kugumuka. Chitsanzo: Nyumbayi ikhoza kudidimuka. Kudikiza (kulindiza): Kudikirira nsima m’makomo mwa eni kuti udye nawo. Chitsanzo: Anapita kukadikiza kwa Anasiyeni. 108