Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 108

Paphata pa Chichewa ntchito m’boma amapita kuntchito kuti akangochongetsa. Akatero amapachita jekete pampando kuti anthu aziona kuti abwera, kenako amapita kukayenda ntchuwa. Kuchotsa akalungusese: Kudyera zankhuli. Chitsanzo: Tiphe bwampini kuti tichotse akalungusese. Kuchotsa mimba: Kupha mwana wosabadwa. Chitsanzo: Mtsikanayu wachotsa mimba. Kuchotsa mimba: Kupha mwana yemwe sanabadwe. Chitsanzo: Azimayi ambiri amapita kuchipatala kuti akachotse mimba. Kuchotsa pakati: Kupha mwana wosabadwa. Chitsanzo: Mtsikanayu wachotsa pakati. Kuchotsa pathupi: Kupha mwana wosabadwa. Chitsanzo: Mtsikanayu wachotsa pathupi. Kuda m’kamwa: Kutukwana. Chitsanzo: Makolo ake ndi akuda mkamwa. Kuda m’manja: Kusauka kwambiri. Chitsanzo: (a) Kadziotche wakeyo ndi ndani yemwe akufu- na kukwatiwa ndi kada m’manja ngati amene uja. (b) Ukada m’manja usaloze zala anzako omwe zikuwayendera. Kuda nkhawa: Kusowa mtendere mumtima chifukwa cha zimene zachitika, zimene ukukumana nazo kapena zimene ukuyembekezera. Chitsanzo: Kuda nkhawa kumayambitsa matenda. (2) Osamada nkhawa ndi zimene sizinachitike, mwina siz- ichitika mkomwe! 107