Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Paphata pa Chichewa | Page 107

Paphata pa Chichewa Chitsanzo: (1) Munthu ameneyu amachita bwino mump- ingo. (2) Munthuyu amachita bwino zinthu. Kuchita dzanzi: (a) Kuzizira kapena kusiya kumva thupi likagwiridwa. Chitsanzo: Mwendo wanga wachita dzanzi. (b) Zochititsa mantha. Chitsanzo: Zimene wachita ndi zochititsa dzanzi. Kuchita nacho: Kudya kapena kumwa. Chitsanzo: Koma alendo aja ndiye achita nayotu nsimayi! Kuchita zazikulu: Kuchita zinthu zolongosoka. Chitsanzo: Akulimbikira maphunziro kuti adzachite zazikulu m’tsogolo. Kuchita zithu mowawanya: Kuchita zinthu mosa- longosoka. Chitsanzo: Anthuwa akuchita zinthu mongowawanya. Kuchita zoopsa: Kukhaulitsa. Chitsanzo: Anamuopseza kuti akadzabweranso adzamuchita zoopsa. Kuchita zopusa: Kugonana. Chitsanzo: Anawapezerera akuchita zopusa. Kuchoka mano: Kutha ntchito, kutsika paudindo, ku- lephera kuchita chinachake. Chitsanzo: (1) Ife tinachoka mano, sitingakwanitse kuchita zimenezi. (2) Likanakhala kale tikanakwanitsa, koma pano tinachoka mano. Kuchongetsa: Kungopitako kuti aone kuti wafika. Chitsanzo: (1) Ndipitako kuti ndikangochongetsa, aka- kandiona ndizikabwerako. (2) Anthu ambiri ogwira 106